Loya Bright Theu wadabwa kuti a Chakwera ndi mkulu wa Polisi sakuyankhulapo za zipolowe

3
Loya Bright Theu wadabwa kuti a Chakwera ndi mkulu wa Polisi sakuyankhulapo za zipolowe
Loya Bright Theu wadabwa kuti a Chakwera ndi mkulu wa Polisi sakuyankhulapo za zipolowe

Africa-Press – Malawi. Mmodzi mwa a katswiri pa nkhani za malamulo mdziko muno a Bright Theu adzudzula mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ndi mkulu wa apolosi mayi Merlyne Yolam ati pokhala chete pamene gulu la zigawenga lakhala likusokoneza ziwonetsero mzinda wa Lilongwe pogwiritsa ntchito zikwanje, mipeni ndi zida zina.

Polemba pa tsamba lawo la mchezo a Theu ati ndizochititsa manyazi kuti a Chakwera ali chete lero pamene ankadzudzula mchitidwe omwewu pa nthawi ya ulamuliro wa chipani cha DPP.

“Ngati mukuwona kuti izi zikuthandizani pa ndale mwalemba mmadzi. Izi ndi zachimidzi” atero a Theu.

Iwo ati pokhala chete mchitidwe wa uchifwambawu ukumera mizu ndipo izi zikubweretsa mantha makamaka pamene dziko lino likuyandira chisankho chaka cha mawa mu September.

For More News And Analysis About Malawi Follow Africa-Press

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here