Africa-Press – Malawi. Pamene chisankho cha pa 16 September chaka chino chikununkhira ngati Mvula yogwera kutali, chipani cha Democratic Progressive (DPP) chatsindika kuti sichikusintha ndipo chilibe malingaliro osintha mtsogoleri wake pa chisankho cha purezidenti komanso wachiwiri wake.
M’neneri wa chipanichi, Shadric Namalomba, wati ndi bodza la mkunkhuniza pa maripoti omwe akumveka kuti chipanichi chikukonza zosintha ochiyimira pa mpando wa purezidenti komanso omutsatira wake.
Kudzera mu chikalata chomwe wasainira m’neneriyu, mphekeserayi ndi yongofuna chabe kusokoneza anthu pamene chisankho chayandikira.
“Tikufuna kunena momveka bwino kuti professor Arthur Peter Mutharika ndiye mtsogoleri wathu pa chisankho cha purezidenti ndipo mwa luntha lake, iye adasankha Justice Dr.Jane Ansah SC kuti akhale omutsatira wake pa chisankhochi,” watero Namalomba.
A Namalomba atsindikanso kuti chisankho cha a Mutharika chotenga a Ansah kukhala otsatira wawo ndi chokhazikika komanso chidalandira madalitso kuchokera kwa atsogoleri a chipanichi, mamembala a chipanichi komanso zipani zomwe ali nazo mu mgwirizano wa chisankho.
“Palibe zokambirana kapena lingaliro loti pakhale kusintha.Mphekeserayi ndi njira imodzi chabe yongofuna kusokoneza anthu,” adatsindika a Namalomba.
Iwo amayankhapo pa nkhani yomwe yatsindikizidwa masiku apitawo mu nyuzipepala ya pa tsamba la intaneti ya Nyasa Times yomwe inalemba kuti chipani cha DPP chakonza zoti a Ansah alowe m’malo mwa a Mutharika ndipo otsatira wawo akhala mtsogoleri wa chipani cha Odya Zake Alibe Mlandu, Michael Usi.
For More News And Analysis About Malawi Follow Africa-Press